7 Ndipo musaturuka pakhomo pa cihema cokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anacita monga mwa mau a Mose.
8 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati,
9 Usamamwa vinyo, kapena coledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'cihema cokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;
10 ndi kuti musiyanitse pakati pa copatulika ndi cosapatulika, ndi pakati pa codetsa ndi coyera;
11 ndi kuti muphunzitse ana a Israyeli malemba onse amene Yehova analankhula nao ndi dzanja la Mose.
12 Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ace otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda cotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulikitsa;
13 ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, locokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza cotero.