1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ace akukhala padera, podwala iye, adzakhalawodetsedwa.
3 Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu adule khungu la mwanayo.
4 Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwace masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwace.