32 Ici ndi cilamulo ca iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pace.
33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
34 Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanu lanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanu lanu;
35 pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.
36 Ndipo wansembe aziuza kuti aturutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse ziri m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;
37 naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ace yakumba kubzola khoma;
38 pamenepo wansembe azituruka ku khomo la nyumba, natseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri;