17 Ndipo cobvala ciri conse, ndi cikopa ciri conse, anagona uipa pamenepo azitsuke ndi madzi, nizidzakhala zodetsedwa kufikira madzulo.
18 Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
19 Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwace nkwa mwazi m'thupi mwace, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo ali yense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
20 Ndipo cinthu ciri conse agonapo pokhala ali padera ncodetsedwa; ndi cinthu ciri conse akhalapo ncodetsa.
21 Ndipo ali yense akhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
22 Ndipo ali yense akhudza cinthu ciri conse akhalapo iye, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
23 Ndipo cikakhala pakama, kapena pa cinthu ciri conse akhalapo iye, atacikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.