14 Usamabvula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wace; ndiye mai wako.
15 Usamabvula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamambvula.
16 Usamabvula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako.
17 Usamabvula mkazi ndi mwana wamkazi wace; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wace, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wace kumbvula; ndiwo abale; cocititsa manyazi ici.
18 Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wace, kumbvuta, kumbvula pamodzi ndi mnzace, akah ndi moyo mnzaceyo.
19 Usamasendera kwa mkazi kumbvula pokhala ali padera cifukwa ca kudetsedwa kwace.
20 Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.