8 Usamabvula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.
9 Usamabvula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.
10 Usamabvula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.
11 Usamabvula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.
12 Usamabvula mlongo wa atate wako; ndiye wa cibale ca atate wako.
13 Usamabvula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako.
14 Usamabvula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wace; ndiye mai wako.