17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
18 Nena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana onse a Israyeli, nuti nao, Ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena wa alendo ali m'Israyeli, akabwera naco copereka cace, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;
19 kuti mulandiridwe, azibwera navo yaimuna yopanda cirema, ya ng'ombe, kapena nkhosa, kapena mbuzi.
20 Musamabwera nayo yokhala ndi cirema; popeza siidzalandirikira inu.
21 Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa cowinda cacikuru, kapena ya pa copereka caufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda cirema.
22 Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapenayodukamwendokapena yopunduka, kapena yapfundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukuru, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto pa guwa la nsembe.
23 Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yocepa ciwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa cowinda siidzalandirika.