30 Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova.
31 Potero muwasunge malamulo anga, ndi kuwacita; Ine ndine Yehova.
32 Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israyeli; Ine ndine Yehova wakukupatulani,
33 amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova.