1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.
3 Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira nchito konse; ndilo sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.
4 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, masonkhano opatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.
5 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, pali Paskha wa Yehova.
6 Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi womwewo ndilo madyerero a mkate wopanda cotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa.
7 Tsiku lace loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena.