4 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, masonkhano opatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.
5 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, pali Paskha wa Yehova.
6 Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi womwewo ndilo madyerero a mkate wopanda cotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa.
7 Tsiku lace loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena.
8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lacisanu ndi ciwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.
9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kuceka dzinthu zace, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;