6 Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi womwewo ndilo madyerero a mkate wopanda cotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda cotupitsa.
7 Tsiku lace loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena.
8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lacisanu ndi ciwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.
9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kuceka dzinthu zace, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;
11 ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata sabata wansembe aweyule.
12 Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonze mwana wa nkhosa wopanda cirema, wa caka cimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.