8 Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.
9 Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la citetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.
10 Ndipo mucipatule caka ca makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muciyese caka coliza lipenga; ndipo mubwerere munthu ali yense ku zace zace, ndipo mubwerere yense ku banja lace.
11 Muciyese caka ca makomi asanuco coliza lipenga, musamabzala, kapena kuceka zophuka zokha m'mwemo; kapenakuceka mphesa zace za mipesa yosadzombola.
12 Popeza ndico caka coliza lipenga; muciyese copatulika, mudye zipatso zace kunja kwa munda.
13 Caka coliza lipenga ici mubwerere nonse ku zace zace.
14 Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana;