18 Ndipo muka panda kundimvera, zingakhale izi ndidzaonjeza kukulangani kasanu nd kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.
19 Popeza ndidzatyola mphamvu yam yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati citsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;
20 ndipo mudzacita nayo mphamvu yanu cabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatse zace, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zace.
21 Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zocimwa zanu.
22 Popeza ndidzatumiza cirombo ca kuthengo pakati pa inu, ndipo cidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nicidzacepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.
23 Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;
24 Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri cifukwa ca zoipa zanu.