2 Lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Munthu akacimwa, osati dala, pa cina ca zinthu ziri zonse aziletsa Mulungu, nakacitapo kanthu;
3 akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kuparamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda cirema, cifukwa ca kucimwa kwace adakucita, ikhale nsembe yaucimo.
4 Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la cihema cokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lace pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.
5 Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwerenao ku cihema cokomanako;
6 ndipo wansembeyo abviike cala cace m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova cakuno ca nsaru yocinga, ya malo opatulika.
7 Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la cofukiza ca pfungo lokoma, lokhala m'cihema cokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la cihema cokomanako.
8 Ndipo acotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yaucimo, acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,