3 Ndipo acotseko, nabwere nao mafuta ace onse; mcira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,
4 ndi imso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso;
5 ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yoparamula.
6 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulikitsa.
7 Monga nsembe yaucimo, momwemo nsembe yoparamula; pa zonse ziwirizi pali cilamulo cimodzi; ikhale yace ya wansembeyo, amene acita nayo cotetezera.
8 Ndipo cikopa ca nsembe yopsereza cikhale cace cace ca wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu ali yense.
9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumcembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi paciwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo,