7 Monga nsembe yaucimo, momwemo nsembe yoparamula; pa zonse ziwirizi pali cilamulo cimodzi; ikhale yace ya wansembeyo, amene acita nayo cotetezera.
8 Ndipo cikopa ca nsembe yopsereza cikhale cace cace ca wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu ali yense.
9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumcembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi paciwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo,
10 Ndipo nsembe zonse zaufa zosanganiza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.
11 Ndipo cilamulo ca nsembe zoyamika, zimene azibwera Daze kwa Yehova ndi ici:
12 akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndinsembe yolemekeza, timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tooca, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.
13 Abwere naco copereka cace pamodzi ndi timitanda ta mkate wacotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zace.