1 NDIPO atafa Yoswa, ana a Israyeli anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?
2 Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lace.
3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkuru wace, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.
4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi.