1 Pamenepo amuna a Efraimu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriraoji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndimotopamtupako.
2 Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukuru ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanju lao.
3 Ndipo pakuona ine kuti simunandipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundicitira nkhondo?
4 Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Gileadi nalimbana naye Efraimu; ndipo amuna a Gileadi anakantha Efraimu, cifukwa adati, Inu Agileadi ndinu akuthawa Efraimu, pakati pa Efraimu ndi pakati pa Manase.
5 Ndipo Agileadi anatsekereza madooko a Yordano a Efraimu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efraimu, Ndioloke, amuna a Gileadi anati kwa iye, Ndiwe M-efraimu kodi? Akati, Iai;
6 pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kuchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordano; ndipo anagwa a Efraimu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.