3 Ndipo pakuona ine kuti simunandipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundicitira nkhondo?
4 Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Gileadi nalimbana naye Efraimu; ndipo amuna a Gileadi anakantha Efraimu, cifukwa adati, Inu Agileadi ndinu akuthawa Efraimu, pakati pa Efraimu ndi pakati pa Manase.
5 Ndipo Agileadi anatsekereza madooko a Yordano a Efraimu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efraimu, Ndioloke, amuna a Gileadi anati kwa iye, Ndiwe M-efraimu kodi? Akati, Iai;
6 pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kuchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordano; ndipo anagwa a Efraimu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.
7 Ndipo Yefita anaweruza Israyeli zaka zisanu ndi cimodzi; nafa Yefita Mgileadi, naikidwa m'mudzi wina wa Gileadi.
8 Ndi pambuyo pace Ibzani wa ku Betelehemu anaweruza Israyeli.
9 Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ace amuna ana akazi makumi atatu ocokera kwina. Ndipo anaweruza Israyeli zaka zisanu ndi ziwiri.