15 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikucedwetseni kuti tikukonzereni mwana wa mbuzi.
16 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undicedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwa kuti ndiye mthenga wa Yehova.
17 Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atacitika mau anu, tikucitireni ulemu.
18 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza liri lodabwitsa?
19 Pamenepo Manowa anatenga mwana wa mbuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anacita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyereo
20 Pakuti kunali, pakukwera lawi la mota pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.
21 Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekeranso kwa Manowa kapena kwa mkazi wace. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova.