19 Pamenepo Manowa anatenga mwana wa mbuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anacita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyereo
20 Pakuti kunali, pakukwera lawi la mota pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wace ali cipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.
21 Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekeranso kwa Manowa kapena kwa mkazi wace. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova.
22 Nati Manowa kwa mkazi wace, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu.
23 Koma mkazi wace ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa pa dzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi yino.
24 Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namucha dzina lace Samsoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.
25 Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.