7 Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samsoni pamaso pace.
8 Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napambuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m'citanda ca mkango munali njuci zoundana, ndi uci.
9 Ndipo anaufula ndi dzanja lace, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wace ndi amai wace, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauza kuti adaufula uciwo m'citanda ca mkango.
10 Ndipo atate wace anatsikira kwa mkazi; ndi Samsoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.
11 Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzace makumi atatu akhale naye.
12 Nanena nao Samsoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kuukumika uwu, ndidzakupatsani malaya a nsaru yabafuta makumi atatu, ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu;
13 koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu Malaya a nsaru yabafuta makumi atatu ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve.