9 Ndipo anaufula ndi dzanja lace, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wace ndi amai wace, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauza kuti adaufula uciwo m'citanda ca mkango.
10 Ndipo atate wace anatsikira kwa mkazi; ndi Samsoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.
11 Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzace makumi atatu akhale naye.
12 Nanena nao Samsoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kuukumika uwu, ndidzakupatsani malaya a nsaru yabafuta makumi atatu, ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu;
13 koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu Malaya a nsaru yabafuta makumi atatu ndi zobvala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve.
14 Ndipo ananena nao,Cakudya cinaturuka m'mwini kudya,Ndi cozuna cinaturuka m'mwini mphamvu,Ndipo masiku atatu sanakhoza kutanthauzira mwambiwo.
15 Koma kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anati kwa mkazi wa Samsoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi mota. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?