20 Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samsoni. Nagalamuka iye m'tulo tace, nati, Ndizituruka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwa kuti Yehova adamcokera.
21 Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi.
22 Koma atammeta tsitsi la pamutu pace linayamba kumeranso.
23 Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikuru, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu m'dzanja lathu.
24 Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.
25 Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samsoni, atisewerere. Naitana Samsoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuika iye pakati pa mizati.
26 Ndipo Samsoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo.