1 Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israyeli; masiku ajanso pfuko la Adani anadzifunira colowa cakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sicinawagwera colowa cao pakati pa mapfuko a Israyeli.
2 Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, a kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efraimu ku nyumba ya Mika, nagona komweko,
3 Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napambukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? ucitanji muno? ukhala naco ciani kuno?
4 Ndipo ananena nao, Mika anandicitira cakuti cakuti, napangana nane za nchito, ndipo ndikhala wansembe wace.
5 Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.
6 Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.
7 Pamenepo amuna asanuwa anacoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhalaokhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakudtitsa manyazi m'cinthu ciri conse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu ali yense.