1 Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israyeli, panali munthu Mlevi wogonera kutseri kwa mapiri a Efraimu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.
2 Koma mkazi wace wamng'ono anacita cigololo akali naye, namcokera kumka ku nyumba ya atate wace ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.
3 Koma anauka mwamuna wace namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wace, ndi aburu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye ku nyumba ya atate wace. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo, anakondwera kukomana naye.
4 Ndipo mpongozi wace, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.