8 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zace zana ndi khumi.
9 Ndipo anamuika m'malire a colowa cace m'Timinatiheresi, ku mapiri a Efraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10 Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena nchitoyi adaicitira Israyeli,
11 Ndipo ana a Israyeli anacita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;
12 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawaturutsa m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.
13 Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti.
14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.