13 Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.
14 Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kucokera ku midzi kumka ku Gibeya, kuti aturuke kulimbana ndi ana a Israyeli.
15 Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'midzi tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala m'Gibeya, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.
16 Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya.
17 Ndipo anawerenga amuna a Israyeli, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okha okha.
18 Nauka ana a Israyeli, nakwera kumka ku Beteli, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.
19 Nauka ana a Israyeli m'mawa, naumangira Gibeya misasa.