17 Ndipo anawerenga amuna a Israyeli, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okha okha.
18 Nauka ana a Israyeli, nakwera kumka ku Beteli, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.
19 Nauka ana a Israyeli m'mawa, naumangira Gibeya misasa.
20 Ndipo amuna a Israyeli anaturuka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israyeli anawandandalikira nkhondo ku Gibeya.
21 Pamenepo ana a Benjamini anaturuka m'Gibeya, naononga a Israyeli tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi,
22 Koma anthu, ndiwo amuna a Israyeli, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.
23 Ndipo ana a Israyeli anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.