30 Ndipo ana a Israyeli anakwerera ana a Benjamini tsiku lacitatu, na nika pa Gibeya monga nthawi zina.
31 Naturuka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israyeli, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kumka ku Beteli, ndi lina ku Gibeya kuthengo.
32 Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israyeli anati, Tithawe, tiwakokere kutari ndi mudzi kumakwalala.
33 Nauka amuna onse a Israyeli m'malo ao nanika ku Baalatamari; naturuka Aisrayeli olalira aja m'malo mwao, m'Maare-geba.
34 Ndipo anadza pandunji pa Gibeya amuna osankhika m'Israyeli monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwa kuti coipa ciri pafupi kuwakhudza.
35 Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israyeli; ndi ana a Israyeli anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.
36 Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israyeli anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibeya.