1 Koma amuna a Israyeli adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wace wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wace.
2 Ndipo anthu anadza ku Beteli, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.
3 Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israyeli, cacitika ici cifukwa ninji m'Israyeli kuti lasowa lero pfuko limodzi m'Israyeli?
4 Ndipo kunali m'mawa mwace, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.
5 Nati ana a Israyeli, Ndani iye mwa mapfuko onse a Israyeli amene sanakwera kudza kumsonkhano kwa Yehova? pakuti panali lumbiro lalikuru pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.
6 Ndipo ana a Israyeli anamva cifundo cifukwa ca Benjamini mbale wao, nati, Pfuko limodzi lalikhidwa pa Israyeli leroli.
7 Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu akazi akhale akazi ao?