10 Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israyeli, naturuka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesapotamiya m'dzanja lace; ndi dzanja lace linamlaka Kusani-Risataimu.
11 Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniveli mwana wa Kenazi anafa.
12 Koma ana a Israyeli anaonjezanso kucita coipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Moabu pa Israyeli, popeza anacita coipa pamaso pa Yehova.
13 Ndipo anadzisonkanitsira ana a Amoni ndi a Amaleki, namuka nakantha Israyeli, nalanda mudzi wa m'migwalangwa nakhalamo.
14 Ndipo ana a Israyeli anatumildra Egiloni mfumu ya Moabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.
15 Koma pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israyeli anatumiza mtulo m'dzanja lace Ikwa Egiloni mfumu ya Moabu.
16 Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konse konse utali wace mkono; nalimangirira pansi pa zobvala zace pa ncafu ya kulamanja.