5 Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Beteli ku mapiri a Efraimu; ndi ana a Israyeli anakwera kwa iye awaweruze.
6 Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?
7 Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magareta ace, ndi aunyinji ace; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.
8 Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.
9 Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzacita nao ulemu; pakuti: Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi, Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.
10 Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafitali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kumka naye.
11 Ndipo Heberi Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wace wa Mose, namanga mahema ace mpaka thundu wa m'Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi.