1 Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba tsiku lomwelo ndi kuti,
2 Lemekezani YehovaPakuti atsogoleri m'Israyeli anatsogolera,Pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.
3 Imvani mafumu inu; cherani makutu, akalonga inu;Ndidzayimbira ine Yehova, inetu;Ndidzamuyimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israyeli,
4 Yehova, muja mudaturuka m'Seiri,Muja mudayenda kucokera ku thengo la Edomu,Dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha,Inde mitambo inakha madzi.