13 Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe catigwera ife bwanji conseci? ndipo ziti kuti zodabwiza zace zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweza kodi Yehova kucokera m'Aigupto? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midyani.
14 Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israyeli m'dzanja la Midyani, Sindinakutuma ndi Ine kodi?
15 Ndipo anati kwa iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israyeli ndi ciani? Taonani, banja langa liri loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.
16 Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidyani ngati munthu mmodzi.
17 Ndipo anati kwa iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse cizindikilo tsopano cakuti ndi Inu wakunena nane.
18 Musacoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kuturutsa copereka canga ndi kuciika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.
19 Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda cotupitsa ya muyeso wa ufa; nyamayi anaiika m'licero, ndi msuzi anauthira mumbale, naturuka nazo kwa iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.