4 nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira cocirira njala m'Israyeli, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena buru.
5 Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kucuruka kwao; iwowa ndi ngamila zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.
6 Ndipo Israyeli anafoka kwambiri cifukwa ca Midyani; ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova.
7 Ndipo kunali, pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova cifukwa ca Midyani,
8 Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;
9 ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;
10 ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.