8 Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.
9 Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.
10 Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;
11 nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wace ku cilekezero ca anthu azidaa m'misasa.
12 Ndipo Amidyani ndi Aamaleki ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'cigwa, kucuruka kwao ngati dzombe; ndi ngamila zao zosawerengeka, kucuruka kwao ngati mcenga wa m'mphepete mwa nyanja.
13 Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzace loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulira-kunkhulira m'misasa ya Midyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala cigwere.
14 Ndipo mnzace anayankha nati, Ici si cina konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yoasi, munthu wa Israyeli; Mulungu wapereka Midyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lace.