4 Ndipo Gideoni anafika ku Yordano, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali cilondolere.
5 Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndirikulondola Zeba ndi Tsalimuna mafumu a Midyani.
6 Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?
7 Ndipo Gideoni anati, Cifukwa cace, Yehova akapereka Zeba ndi Tsalimuna m'dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m'cipululu ndi mitungwi.
8 Ndipo anacokapo kukwera ku Penueli, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penueli anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.
9 Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penueli ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi.
10 Zeba ndi Tsalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.