1 Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nacitira Ai ndi mfumu yace monga adacitira Yeriko ndi mfumu yace; ndi kuti nzika za Gibeoni zinacitirana mtendere ndi Israyeli, nizikhala pakati pao;
2 anaopa kwambiri, popeza Gibeoni ndi mudzi waukuru, monga wina wa midzi yacifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwace, ndi amuna ace onse ndiwo amphamvu.
3 Cifukwa cace Adoni-Zedeki anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piraniu mfumu ya Yarimutu, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Dibri mfumu va Egiloni, ndi kuti,
4 Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibeoni, pakuti unacitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israyeli.
5 Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimutu, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibeoni, nauthira nkhondo.
6 Ndipo amuna a ku Gibeoni anatumira Yoswa mau kucigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.