1 Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazoro anacimva, anatwna kwa Yabobu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akasafu,
2 ndi kwa mafwnu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kucigwa kwumwela kwa Kineroto, ndi kucidikha, ndi ku mitunda ya Doro kwnadzulo;
3 kwa Akanani kwn'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Herimoni, m'dziko la Mizipa.
4 Ndipo anaturuka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kucuruka kwao ngati mcenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magareta ambirimbiri.
5 Ndipo mafwnu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israyeli nkhondo.