1 Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israyeli anwakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordano kum'mawa, kuyambira cigwa ca Arimoni, mpaka phiri la Herimoni, ndi cidikha conse ca kum'mawa;
2 Sihoni mfumu ya Aaroori wokhala m'Hesiboni, wocita ufumu kuyambira ku Aroeri ndiwo m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi pakati pa cigwa ndi pa Gileadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
3 ndi pacidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kucidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere kum'mawa, njira ya Beti-Yesimoti; ndi kumwela pansi pa matsikiro a Pisiga.
4 Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basana wotsala wa Arefai, wokhala ku Asitarotu ndi ku Edrei,
5 nacita ufumu m'phiri la Herimoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basana lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Gileadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.