29 Mose anaperekanso colowa kwa pfuko la Manase logawika pakati, ndico ca pfuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao.
30 Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basana lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basana, ndi midzi yonse ya Yairi, yokhala m'Basana, midzi makumi asanu ndi limodzi;
31 ndi Gileadi logawika pakati, ndi Asitarotu ndi Edrei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basana, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.
32 Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m'zidikha za Moabu, tsidya ilo la Yordano ku Yeriko, kum'mawa.
33 Koma pfuko la Levi, Mose analibe kulipatsa colowa: Yehova Mulungu wa lsrayeli, ndiye colowa cao, monga ananena nao.