13 ndi pocoka pamenepo anapitirira kumka kum'mawa ku Gati-heferi, ku Etikazini; naturuka ku Remoni umene ulembedwa mpaka ku Nea,
14 nauzungulira malire kumpoto, kumka ku Hanatoni; ndi maturukiro ace anali ku cigwa ca Ifita-eli;
15 ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.
16 Ici ndi colowa ca ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
17 Maere acinai anamturukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.
18 Ndi malire ao anali ku Yezireeli, ndi Kesulotu, ndi Sunemu;
19 ndi Hafaraimu, ndi Sioni, ndi Anaharati;