5 ndi Zikilaga, ndi Beti-malikabotu, ndi Hazari-susa:
6 ndi Beti-lebaotu, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi miraga yao;
7 Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asana; midzi inai ndi miraga yao;
8 ndi miraga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalata-beeri ndiwo Rama kumwera. Ndico colowa ca pfuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.
9 M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.
10 Ndipo maere acitatu anakwecera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a colowa cao anafikira ku Saridi;
11 nakwera malire ao kumka kumadzulo ndi ku Marala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokineamu;