1 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lace Rahabi, nagona momwemo.
2 Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israyeli, kulizonda dziko.
3 Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Turutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.
4 Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;
5 ndipo m'mene akadati atseke pacipata, kutada, anaturuka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.