1 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,
2 Nena ndi ana a Israyeli ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose,
3 kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalira inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.
4 Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa cipata ca mudziwo, nafotokozere mlandu wace m'makutu a akuru a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.
5 Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.
6 Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.