29 Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa cihema cace.
30 Pamene Pinehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akuru a mabanja a Israyeli okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.
31 Ndipo Pinehasi, mwana wa Eleazare wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, Lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira naco Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israyeli m'dzanja la Yehova.
32 Ndipo Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe, ndi akalonga anabwerera kucokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Gileadi, kudza ku dziko La Kanani kwa ana a Israyeli, nawabwezera mau.
33 Ndipo mauwo anakomera ana a Israyeli pamaso pao; ndi ana a Israyeli analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi.
34 Ndipo ana a Rubeni ndi: ana a Gadi analicha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.