8 koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munacita mpaka lero lino.
9 Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikuru ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.
10 Munthu mmodzi wa inu adzapitikitsa anthu cikwi cimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.
11 Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.
12 Koma, mukadzabwereram'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;
13 dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.
14 Ndipo taonani, lero lino ndirikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mau amodzi; onse anacitikira inu, sanasowapo mau amodzi.