7 munene nao, Cifukwa madzi a Yordano anadulidwa patsogolo pa likasa la cipangano ca Yehova; muja lidaoloka Yordano, madzi a Yordano anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala cikumbutso ca ana a Israyeli cikhalire.
8 Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli; ndipo anaoloka nayo kumka kogona, naiika komweko.
9 Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la cipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.
10 Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordano, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.
11 Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.
12 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la pfuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israyeli, monga Mose adanena nao;
13 ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.