1 Koma ana a Israyeli analakwa ndi coperekedwaco; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda, anatapa coperekedwaco; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israyeli.
2 Ndipo Yoswa anatuma amuna kucokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Beti-aveni, kum'mawa kwa Beteli; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.
3 Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka;
4 Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai.
5 Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapitikitsa kuyambira pacipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.
6 Ndipo Yoswa anang'amba zobvala zace, nagwa nkhope yace pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akulu akulu a Israyeli, nathira pfumbi pamitu pao.
7 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordano, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordano!